Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 33:7 - Buku Lopatulika

7 Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu, amakundika zakudya mosungiramo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu, amakundika zakuya mosungiramo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adasonkhanitsa pamodzi madzi a m'nyanja zakuya ndipo adaziikira malire kuti zisasefukire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 33:7
11 Mawu Ofanana  

Analembera madziwo malire, mpaka polekeza kuunika ndi mdima.


Anagawa nyanja nawapititsapo; naimitsa madziwo ngati khoma.


Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja.


Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu.


Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa