Genesis 1:9 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. Onani mutuwoBuku Lopatulika9 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pakumwamba asonkhane pamodzi pamalo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Mulungu adatinso, “Madzi apansiŵa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. Onani mutuwo |
Kodi simuyenera kuchita nane mantha?” Akutero Yehova. “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga? Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo. Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo; mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.