Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Eksodo 40:23 - Buku Lopatulika Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo pamwamba pa tebulolo adaikapo buledi, monga momwe Chauta adamlamulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi.
Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.
Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.