Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 24:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Muŵaike m'mizere iŵiri pa tebulo la golide wabwino kwambiri, mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Muwayike pa tebulo la golide wabwino kwambiri pamaso pa Yehova mʼmizere iwiri. Mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 24:6
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera;


nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;


kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.


Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo;


Ndipo uziika mkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.


gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;


Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.


Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.


Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa