Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu adaamanga chihema, ndipo m'chipinda chake choyamba munkakhala choikaponyale, tebulo, ndi mikate yoperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa “Malo Opatulika.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:2
21 Mawu Ofanana  

Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.


Ndipo uziika mkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.


Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;


Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.


Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri.


Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.


Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro,


Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake aamuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.


Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.


Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo.


kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa