Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 40:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo anaika choikapo nyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 M'chihema chamsonkanomo adaikamo choikaponyale mopenyana ndi tebulo chakumwera kwake kwa malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 40:24
13 Mawu Ofanana  

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.


Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.


Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.


Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu.


Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikire.


Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi.


Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa