Mateyu 12:4 - Buku Lopatulika4 Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo kunali kosaloledwa kuti iyeyo kapena anzakewo nkumudya, koma ansembe okha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha. Onani mutuwo |