Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 12:5 - Buku Lopatulika

5 Kapena simunawerenge kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe mu Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Kapena simunawerenga kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Kaya simudaŵerengenso m'Malamulowo kuti m'Nyumba ya Mulungu, pa tsiku la Sabata, ansembe amaphwanya lamulo lokhudza tsiku la Sabata, komabe saŵayesa olakwa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 12:5
7 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata?


Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga.


Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa