Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.
Eksodo 39:32 - Buku Lopatulika Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ntchito yonse yomanga chihema chamsonkhano idatha. Aisraele aja adachitadi zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.
Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga ntchito yonse anaichitira mfumu Solomoni ya m'nyumba ya Yehova.
Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.
Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.
chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho;
Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake;
pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.
Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.