Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
Eksodo 38:8 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adapanga beseni lamkuŵa losambira, pamodzi ndi phaka lake. Adapanga zimenezi ndi akalilole a akazi amene ankatumikira ku chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano chija, kumene Chauta ankakumanako ndi anthu ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano. |
Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.
Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.
Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;
Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.
Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.
zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana.
Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai.
koma Petro anaima kukhomo kunja. Chifukwa chake wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro.
Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:
ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako.