Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 4:2 - Buku Lopatulika

2 Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pambuyo pake adapanga thanki. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu, ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 4:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni.


Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.


Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.


Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.


Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.


Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.


zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa