2 Mbiri 4:1 - Buku Lopatulika1 Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Solomoni adapanga guwa lamkuŵa, m'litali mwake mamita asanu ndi anai, m'mimba mwake asanu ndi anainso, ndipo msinkhu wake pafupi mamita anai ndi theka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka. Onani mutuwo |
Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.