Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 26:69 - Buku Lopatulika

69 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

69 Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

69 Petro adaakhala kunja m'bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

69 Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:69
18 Mawu Ofanana  

Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya?


Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya?


Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.


Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya.


Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;


Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro.


Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa.


Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.


Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone.


Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka mu Galileya?


Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka mu Galileya? Santhula, nuone kuti mu Galileya sanauke mneneri.


Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa