Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la chihema cha Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako.
Eksodo 38:1 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake adapanga guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutali mwake munali masentimita 229, muufupi mwakenso ngati masentimita 229 mbali zonse zinali zofanana, msinkhu wake ngati masentimita 137. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. |
Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la chihema cha Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako.
Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi.
ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;
Ndipo anapanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zinakhala zotuluka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.
Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.
Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;
koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.