Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 37:29 - Buku Lopatulika

29 Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosanganiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Adapanganso mafuta oyera odzozera, ndiponso zofukizira za fungo lokoma. Mapangidwe ake adachita monga momwe ankachitira mmisiri wopanga zonunkhira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 37:29
18 Mawu Ofanana  

Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.


Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.


Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano.


Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,


Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide.


Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.


Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo.


Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse.


Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa