Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 38:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake adapanga guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutali mwake munali masentimita 229, muufupi mwakenso ngati masentimita 229 mbali zonse zinali zofanana, msinkhu wake ngati masentimita 137.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 38:1
19 Mawu Ofanana  

Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko.


Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka.


zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha;


Ndipo Yehova anati kwa Mose,


guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake,


Anapanga nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo, kotero kuti nyangazo ndi guwalo zinali chinthu chimodzi, ndipo anakuta guwalo ndi mkuwa.


Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.


“Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano.


Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja.


Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.


Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo.


Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.


Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.


nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.


inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.


Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa