Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:14 - Buku Lopatulika

14 koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:14
76 Mawu Ofanana  

Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi?


Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.


Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.


Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.


Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwanawang'ombe wopanda chilema, ndipo uyeretse malo opatulika.


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.


Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema;


Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.


Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;


Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.


Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?


Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha,


Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!


Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wakuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono?


Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,


Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso.


kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha;


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:


ndipo sanalekanitse ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro.


Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;


amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu;


Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?


Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wakuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?


ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.


Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha.


Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.


Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu.


tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.


Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.


Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine!


Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.


Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?


Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,


Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.


kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.


koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire;


Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pamutu wa ndodo yake.


Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka;


amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha.


kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.


chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo;


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;


kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa