Eksodo 36:10 - Buku Lopatulika Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo adasokerera nsalu zisanu, kuti zikhale chinsalu chimodzi, zisanu zinazonso adazisokerera nkukhalanso chinsalu chimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. |
Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake.
Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri.
Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao.
Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi.
Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho.
kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;
Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu;