Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Eksodo 27:20 - Buku Lopatulika Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uŵalamule Aisraele kuti akupatse mafuta aolivi opsinyidwa bwino, oyatsira nyale, kuti ziziyaka kosalekeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. |
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Zipangizo zonse za chihema, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa.
ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.
ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma;
choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.
Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?
ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.