Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 11:4 - Buku Lopatulika

4 Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mboni ziŵirizo ndi mitengo iŵiri ija ya olivi, ndi ndodo za nyale ziŵiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye olamulira dziko lonse lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 11:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.


Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi.


Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.


Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka.


Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wakuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,


Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa