Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:19 - Buku Lopatulika

19 Zipangizo zonse za chihema, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Zipangizo zonse za Kachisi, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Zipangizo zonse zogwiritsira ntchito zosiyanasiyana m'chihemamo, pamodzi ndi zikhomo za chihemacho ndi za bwalolo, zonsezo zikhale zamkuŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Zipangizo zonse zogwiritsa ntchito zosiyanasiyana pa chihemacho, zikhomo za chihema ndi zabwalolo zikhale zamkuwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:19
14 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono mu ukapolo wathu.


Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa.


Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.


Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa.


zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao;


Ndi zichiri zonse za chihema, ndi za bwalo lake pozungulira, nza mkuwa.


ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira.


nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako;


Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.


Tayang'ana pa Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.


Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi.


ndi nsichi za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake.


ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa