Eksodo 25:9 - Buku Lopatulika Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha Kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Umange chihemacho monga m'mene ndidzakulangizire mapangidwe ake ndiponso mapangidwe a katundu yense wam'menemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere. |
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
Natenge zipangizo zake zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsalu yamadzi, ndi kuziphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pachonyamulira.
Ndipo mapangidwe ake a choikaponyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikaponyali.
Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.
Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.
amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.
Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.
ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.