Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Eksodo 23:8 - Buku Lopatulika Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. |
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
amene m'manja mwao muli mphulupulu, ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.
Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga, kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.
Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano.
Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;
Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusakaniza zakumwa zaukali;
Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.
Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.
Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.
Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.
Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.