Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:3 - Buku Lopatulika

3 Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndi akatswiri pochita zoipa. Akalonga ndi aweruzi amafuna ziphuphu, ndipo mtsogoleri amaŵauza zoipa zimene afuna kuti iwo achite. Motero amalakwira pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:3
26 Mawu Ofanana  

Wotsinzina ndiye aganizira zokhota; wosunama afikitsa zoipa.


Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga, kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.


Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.


Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala padziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.


Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa.


Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.


amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake!


Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.


Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


Taona akalonga a Israele, yense monga mwa mphamvu yake, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi.


Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo,


Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.


Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri.


Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.


Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.


Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;


nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa