Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.
Eksodo 22:24 - Buku Lopatulika ndi mkwiyo wanga udzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi mkwiyo wanga idzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo. |
Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.
Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa, ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.
pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.
Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.
Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.
Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.
Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.
Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.
Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.
Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako.