Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 15:8 - Buku Lopatulika

8 Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Akazi amasiye ndidaŵachulukitsa, kupambana mchenga wakunyanja. Amai ndidaŵaonongera ana ao akali anyamata abiriŵiri. Mwadzidzidzi ndidaŵagwetsera chisoni ndi nkhaŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndinachulukitsa amayi awo amasiye kupambana mchenga wa kunyanja. Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna dzuwa lili pamutu. Mwadzidzidzi ndinawagwetsera kuwawa mtima ndi mantha.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 15:8
15 Mawu Ofanana  

Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m'nkhondo.


Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.


Pakuti Yehova atero za ana aamuna ndi za ana aakazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:


Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.


Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zake; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto.


Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera mizinda ya Yuda mau ao.


Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'mizinda mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka.


Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.


Ndife amasiye opanda atate, amai athu akunga akazi amasiye.


Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.


Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.


pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa