Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 69:24 - Buku Lopatulika

24 Muwatsanulire mkwiyo wanu, ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Muwatsanulire mkwiyo wanu, ndipo moto wa ukali wanu uwagwere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Muŵagwetsere ukali wanu, mkwiyo wanu woyaka moto uŵagwire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo; mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 69:24
14 Mawu Ofanana  

Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu, ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.


Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa