Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.
Eksodo 19:15 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kenaka Mose adaŵauza kuti, “Mkucha uno, mukonzeke. Musayandikize mkazi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.” |
Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera.
Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.
Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.
Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.
Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele.
nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri?
Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;
Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.