Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:44 - Buku Lopatulika

44 Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Inunso tsono muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa nthawi imene inu simukumuyembekezera.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:44
11 Mawu Ofanana  

Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.


Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.


Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.


Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.


Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza.


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.


Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.


Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa