Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:43 - Buku Lopatulika

43 Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Koma zindikirani ichi: Ngati mwini nyumba akanadziwa nthawi yanji ya usiku imene mbala imabwera, sakanagona ndipo sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:43
18 Mawu Ofanana  

Kuli mdima aboola nyumba, usana adzitsekera, osadziwa kuunika.


Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali;


Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja.


Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja,


Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.


Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza.


Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo.


Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake.


Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;


Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;


Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.


Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)


Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa