ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
Eksodo 17:6 - Buku Lopatulika Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe mu Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. |
ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi.
Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mzinda wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba.
Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako ndi mitsinje inasefuka; kodi adzakhozanso kupatsa mkate? Kodi adzafunira anthu ake nyama?
Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba.
Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma.
Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.
Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.
Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo.
koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha.
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.
Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.
amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;
Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.