Numeri 20:8 - Buku Lopatulika8 Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 “Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mbale wako Aroni musonkhanitse mpingo, tsono ulamule thanthwe kuti litulutse madzi, anthu akuwona. Motero udzaŵatulutsira madzi m'thanthwe anthuwo, ndipo udzamwetsa mpingo wonsewo ndi zoŵeta zao zomwe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mʼbale wako Aaroni musonkhanitse anthu onse pamodzi. Uyankhule ndi thanthwe ilo iwo akuona ndipo lidzatulutsa madzi ake. Udzatulutsa madzi mʼthanthwe limeneli kuti anthu onse ndi ziweto zawo amwe.” Onani mutuwo |