Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Eksodo 15:5 - Buku Lopatulika Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nyanja yozamayo idaŵaphimba onse, adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.” |
Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.
Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.
Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.
Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya.
koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.
Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mzinda waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.