Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Eksodo 10:3 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose ndi Aroni adapita kwa Farao kukamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Ahebri, akufunsa kuti, ‘Kodi udzakanabe kundigonjera mpaka liti? Uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze. |
Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.
Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.
popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.
Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.
popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.
ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira;
Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.
Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.
Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.
Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.
Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetse m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse;
Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.
Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;