Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 13:18 - Buku Lopatulika

18 Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Uza mfumu pamodzi ndi mai wake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumu, poti zisoti zanu zokongola zaufumu zagwa pansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumuyo, pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo zagwa pansi.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:18
30 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.


Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.


Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.


Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.


Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,


pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.


ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri;


Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi.


Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka.


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiremo; m'menemo udzafa.


anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,


Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse.


Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni; akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa, anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.


Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukire chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.


Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.


Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa.


Momwemo ndinaika chipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako.


atero Ambuye Yehova, Chotsa chilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, chepsa chokwezeka.


Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu.


Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake.


Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'chuuno mwao; asavale m'chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta.


Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake;


Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.


Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.


Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.


Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa