Danieli 5:9 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho mfumu Belisazara anachita mantha koposa ndipo nkhope yake inapitirira kusinthika. Akalonga ake anathedwa nzeru. |
Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.
Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya aakuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine.
Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.
Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.
Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;