Yeremiya 30:6 - Buku Lopatulika6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Funsani kuti muzindikire, Kodi munthu wamwamuna angathe kubala mwana? Nanga nchifukwa chiyani ndikuwona munthu wamwamuna aliyense atagwira manja pa mimba ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope zonse zagwa? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti: Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa? Onani mutuwo |