Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 2:1 - Buku Lopatulika

1 Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 2:1
14 Mawu Ofanana  

Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.


Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni;


Niti nao mfumu, Ndalota loto, nuvutika mzimu wanga kudziwa lotolo.


Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba.


Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine.


Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru.


Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira.


Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule.


Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa