Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
Aefeso 2:3 - Buku Lopatulika amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. |
Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti.
Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.
Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.
Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?
Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.
ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.
amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;
Pakuti monga inunso kale simunamvere Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,
Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo;
Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.
Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo.
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake:
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza.
Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.
zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;
Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.
Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala.