Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 8:1 - Buku Lopatulika

Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake Davide adathira nkhondo Afilisti, naŵagonjetsa, ndipo adaŵalanda mzinda wa Metegama.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndi kuwapambana ndipo analanda Metegi Ama kuchoka mʼmanja mwa Afilistiwo.

Onani mutuwo



2 Samueli 8:1
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.


Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, panjira ya ku chipululu cha Gibiyoni.


Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.


Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja.


Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere.


Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.


Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu; mwandiika mutu wa amitundu; mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.


Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.


Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.


amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele.