Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwachita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikulu izi zonse.
2 Samueli 7:21 - Buku Lopatulika Chifukwa cha mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munachita ukulu wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munachita ukulu wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwachita zazikulu zonsezi chifukwa cha lonjezo lanu, ndiponso potsata zimene mtima wanu umafuna, kuti mtumiki wanune ndidziŵe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu. |
Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwachita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikulu izi zonse.
Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu.
Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo,
Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,
monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu:
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.