Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
2 Samueli 5:10 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, anali naye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. |
Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;
Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere.
Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.
Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.
Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.
Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;
Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.
Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe.