2 Samueli 5:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Onani mutuwoBuku Lopatulika10 Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, anali naye. Onani mutuwo |
Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.