Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hagai 2:4 - Buku Lopatulika

4 Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Komabe Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, usataye mtima iwe Zerubabele, usataye mtima iwe Yoswa, mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, musataye mtima inu nonse. Yambani ntchito, pakuti Ine ndili nanu ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Hagai 2:4
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.


Momwemo udzalemerera, ukasamalira kuchita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israele; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.


Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova.


Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi achilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake Maaseiya, ndi Eliyezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.


Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.


Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo mu Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.


Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, mu uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.


Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.


Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe.


Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen.


Ndipo makolo aakuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,


Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe.


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.


Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.


Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.


Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.


Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa