mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
2 Samueli 4:9 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Davide adayankha Rekabu ndi Baana mbale wake kuti, “Ndithu pali Chauta wamoyo, amene waombola moyo wanga kwa adani anga onse, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse, |
mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati padziko lapansi.
Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;
Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse,
Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.
Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.
Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.