Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Isibosetiyo anali ndi anthu aŵiri amene anali atsogoleri a magulu ankhondo. Wina anali Baana, wina anali Rekabu, onsewo ana a Rimoni, wa fuko la Benjamini, wa ku Beeroti (pakuti Beeroti ndi chigawo cha Benjamini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini,

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 4:2
9 Mawu Ofanana  

Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya;


Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere.


Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana.


Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse,


Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu.


Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele.


Gibiyoni ndi Rama, ndi Beeroti;


ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza;


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa