ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
2 Samueli 3:1 - Buku Lopatulika Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kunali nkhondo nthaŵi yaitali pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide. Davide mphamvu zake zinkakulirakulira pamene anthu a Saulo ankafookerafookera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera. |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abinere ndi anthu a Israele anathawa pamaso pa anyamata a Davide.
Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso.
Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.
Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo.
Ana a Davide tsono ombadwira ku Hebroni: woyamba Aminoni wa Ahinowamu wa ku Yezireele, wachiwiri Daniele wa Abigaile wa ku Karimele,
Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamgonjetsa; koma udzagwada pamaso pake.
Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.
Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono, chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.
Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu; mwandiika mutu wa amitundu; mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.
Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto.
Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wogonjetsa kuti akagonjetse.