Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Davide anakulakulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Davide anakulakulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta wamphamvuzonse anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere.


Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye.


Ndipo anamanga mzinda pozungulira pake, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pake; ndi Yowabu anakonzanso potsala pa mzinda.


ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.


Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe.


Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa