2 Samueli 22:5 - Buku Lopatulika Pakuti mafunde a imfa anandizinga, mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mafunde a imfa anandizinga, mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Zoŵaŵa za imfa zidandizinga, mitsinje ya ku malo a anthu akufa idandisefukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri. |
Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.
Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira.
Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.
Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,
Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.