Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 17:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pamadzi ambiri,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 17:1
20 Mawu Ofanana  

Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.


Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama.


Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.


Iwe wokhala pamadzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako.


Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse yakuthengoko.


Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?


Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;


Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane;


Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika mu Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.


pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.


Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.


Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake.


Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.


Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka mu Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa